Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 4

Paphata pa Chichewa Adawatulukira: (a) Adawachezera Chitsanzo: Atabwera kuno anapita kukawatulukira agogo. (b) Anazindikira chinyengo chawo. Chitsanzo: Adawatulukira kuti amanena bodza. Adzukulu: Anthu okumba manda komanso kuika maliro, mawuwa amatanthauzanso ana a mwana wako. Chitsanzo: Adzukuluwo anagwira wanjinga n’kumumangirira pamtengo pofuna kumupatsa phunziro kuti asadzadutsenso pamanda atakwera njinga. Agwireni ntchito: Amenyeni. Chitsanzo: Anyamata aja ndi amenewa, agwireni ntchito. Akadayenda: Ali ndi pakati koma sanachirebe. Chitsanzo: “Kodi ali ndi mwana tsopano?” “Ayi akadayenda.” Akalimbalimba: Akachita makani. Chitsanzo: Akakalimbalimba mukangomumanga. Akamwiniatsatana: Kagulu ka nyenyezi zisanu zowala bwino. Chitsanzo: Wawaona akamwiniatsatana? Akapamba okhala pachifu: Anthu osauka kwambiri, osowa pokhala. Chitsanzo: Ife ndiye ndi akapamba okhala pachifu, angatiwerengere ife! Akucheperakaba: Ndi mwana. Chitsanzo: Amene uja akucheperakaba, sangandimenye. Akuchita nseru: Akufuna kusanza. Chitsanzo: Mwanayu akuchita nseru. 3