Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 399

Paphata pa Chichewa Zibolobosha: Kulemba zinthu zosaoneka bwino. Chitsanzo: Amangolemba zibolobosha. Zidze pano n’zatonse: Mavuto akagwa timafunika kuthandizana. Chitsanzo: Adwala kwambiri moti m’pofunika kulimba mtima. Zidze pano n’zatonse! Zifuyo: Ziweto. Nthawi zina mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za agalu oweta. Akakhala ambiri ena amangowanena kuti zifuyo. Chitsanzo: Pakhomo pawo pali zifuyo. Zigogodo: Zibakera, nthawi zambiri mawuwa amanena za munthu wokonda ndewu. Chitsanzo: Amuthamitsa anzake odziwa zigogodo. Zijazi: Mawu omwe ena amanena ngati sakufuna kutchula zinthu zinazake kapena ngati zinthuzo zili zachinsinsi. Chisanzo: Ubwere pa nthawi ya nkhomaliro, koma usaiwale zijazi. Zikhulupiriro zachikuda: Mawu amenewa amanena za kukhulupirira za ufiti, matsenga komanso mizimu. Anthu ambiri a ku Africa kuno amakhulupirira zimenezi chifukwa ndi zimene makolo awo akhala akuzikhulupirira. Chitsanzo: Pamene amishonale ankabwera, anapeza anthu akuda ali ndi miyambo yawo ndipo anayamba kunena kuti zikhulupiriro zachikuda n’zosemphana ndi mawu a Mulungu. Zikusuntha? Zili bwino, zikuyenda bwino. Chitsanzo: Ife zikungoyenda ngati nkhono, inu bwanji, zikusuntha? Zikuwayendera: Sakukumana ndi mavuto. Chitsanzo: Kungoona mmene akuonekera ukumadziwiratu kuti zikuwayendera. 398