Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 398
Paphata pa Chichewa
Zayakunkhongo: Munthu wosamva za anzake,
wosamvera.
Chitsanzo: (1) Kodi zayakunkhongo uja ali kuti? (2)
Ngakhale mumulangize saamva. Iye uja ndi
zayakunkhongo.
Zayakunkhongo: Munthu wosamva.
Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi zayakunkhongo,
ngakhale mumuuze saamva.
Zayang’ana kungolo: Zavuta. Mawuwa amayerekezera
zimene zimachitika ng’ombe zikayang’ana kungolo.
Chitsanzo: Atangotulukira ndinadziwa kuti zayang’ana
kungolo.
Zazii: Zopanda nzeru.
Chitsanzo: Anabwera kunoko n’kumandiuza zazii.
Zazira: Kalipira.
Chitsanzo: Mukamasokosera akuzazirani.
Zedi: Kuvomereza kuti ndi zoona, ndithu.
Chitsanzo: Zedi, akunenadi zoona.
Zembeneku: Kuthawa mofulumira.
Chitsanzo: Anangoti zembeneku!
Zemberana: Chita zachimasomaso, chita uhule.
Chitsanzo: Bambo a pamtunda aja amazemberana ndi
mlamu wawo.
Zembetsa: Thawitsa mobisa, kulowetsa katundu
mwachinyengo.
Chitsanzo: (1) Ndani wazembetsa katunduyu? (2) Anthu
ena akumazembetsa katundu waboma.
Zembetsana: Kutengana mopanda dongosolo
n’kumakhala ngati banja.
Chitsanzo: Anazemetsana ndi mwamuna wamwini.
Zibalobalo: Zipatso za mtengo. Nthawi zambiri
sizidyedwa.
Chitsanzo: Apulula zibalobalo zonse.
397