Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 397

Paphata pa Chichewa Zangazilipaphiri: Munthu womana kapena woumira. Chitsanzo: Mwamuna wawo ndi zangazilipaphiri. Zankhaninkhani: Zambirimbiri. Chitsanzo: Ali ndi ndalama zankhaninkhani. Zanoninoni (zonona): Za mafuta. Chitsanzo: Tadyera ndiwo zanoninoni (zonona). Zantchito: (a) Mawuwa amanenedwa ngati munthu akufuna kuchita khama pochita zinazake kapena akamalimbikitsa ena kuchita khama. Chitsanzo: (1) Ndikufuna kulima zantchito. (2) Anyamata tiyeni, zantchito! (b) Mawuwa amanenedwa wina akachitiridwa zinazake mwamphamvu kapena mankhanza. Chitsanzo: Anzake amumenya zantchito! Zapana: Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti mbuzi zadya. Chitsanzo: Mbuzizi zapana, pitani mukazilowetse. Zatera pa uta: Zadzidzimutsa. Chitsanzo: Mavutowatu atera pa uta. Zathasalala: Zafulati. Chitsanzo: Chitumbuwacho chikhale chathasalala. Zathina: Zavuta. Chitsanzo: (1) Mabwenzi enieni amaoneka zinthu zikathina. (2) Ataona kuti zathina, anathawa. Zatifiiritsa maso: Zatipanikiza. Chitsanzo: Mavuto atifiiritsa maso. Zatswayitswayi: Nyama kapena zinazake zankhuli. Chitsanzo: Ofunika lero tidyeko zatswayitswayi. Zawamba: Zachisawawa, zopezeka mosavuta. Chitsanzo: Amavala zovala zawamba. 396