Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 396

Paphata pa Chichewa Zakuvuta: Walephera. Chitsanzo: Ngati umaganiza kuti undipusitsa, zakuvuta! Zam’kutu: Zopanda nzeru, zosathandiza. Chitsanzo: Nditakumana naye anayamba kundiuza zam’kutu. Zam’maluwa: Zabodza, zopanda pake. Chitsanzo: Akukuuzanizi ndi zam’maluwa. Zam’manja: Ndalama. Chitsanzo: Anamulonjeza kuti amupatsa zam’manja. Zam’mutu: Kuyankhula zopanda nzeru. Chitsanzo: Zimene akuyankhula ndi zam’mutu. Zamadulira: Zachidule. Chitsanzo: Amayenda zamadulira, wakumana nazo. Zambwerera: Zopusa. Chitsanzo: Munthu wanzeru sayankhula zambwerera. Zamoyo palibe: Zokayikitsa ngati atachire. Chitsanzo: Apatu zamoyo ndiye palibe. Zamtopola: Zachipongwe. Chitsanzo: Anyamatawa akupitirizabe kuchita zamtopola. Zamugwera: Wakumana ndi vuto. Chitsanzo: Mnzanu uja zamugwera. Zamwaanthu: Mavuto otumizidwa ndi anthu mosadziwika bwino. Mawu amenewa amanenedwa chifukwa cha zikhulupiriro zoti anthu ena amatha kulodza anzawo. Chitsanzo: Ndi zamwaanthu izi, si mwati kuchipatala sanakupezeni ndi matenda? Zandisuntha: Zandikhudza, zandigwira mtima. Chitsanzo: Nkhani ya mnyamatayo yandisuntha. Zandithyola nkhongono: Zandifooketsa kwambiri. Chitsanzo: Nkhaniyi yandithyola nkhongono. 395