Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 394

Paphata pa Chichewa Yokoka ngolo: Mawu amenewa amatanthauza kuti ndi nyama yolimba. Nthawi zambiri nyama imene imakoka ngolo imakhala yolimba mnofu kwambiri. Chitsanzo: Nyamayi inali yokoka ngolo. Yophera awemba: Bodza lomwe munthu amanena kapena zinthu zina zomwe munthu amachita pofuna kupusitsa mnzake. Mawuwa angananenso zinthu zimene wina angachite ngati pongobisalira zolinga zake zili zina. Chitsanzo: Mumaganiza kuti ndikudwaladi, inali yophera awemba! Yosagwira: Zoti sizingathandize, si zomveka. Chitsanzo: Imeneyo ndi yosagwira, sindingatsuke mbale komanso kukolopa m’nyumba iweyo uli khale! Yosipa (wosipa): Kudya nsoma yopanda ndiwo. Chitsanzo: Akudya nsima yosipa. Yotentha: Yopezetsa ndalama. Chitsanzo: Ayamba bizinezi yotentha. Yudasi: Munthu amene amam’pereka mnzake ngati mmene anachitira mwini dzinali. Chitsanzo: Munthu ameneyu ndi Yudasi ndithu, osamumvera chisoni mnzake? 393