Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 392

Paphata pa Chichewa Yedzeka: Kutula pansi, kuyedzamiritsa kamtengo. Chitsanzo: Yedzekani katunduyo apa. Yenda chining’a: Kuchita chinyengo. Chitsanzo: Kodi nanunso mwayamba kuyenda chining’a. Yenda chogona: Mwalira. Chitsanzo: Mudzandilira ndikadzayenda chogona. Yenda m’mapazi: Kuzonda munthu, kukulondalonda. Chitsanzo: Sindingamacheze nawo chifukwa amandiyenda m’mapazi. Yenda mahala: Kusapeza chomwe umayendera. Chitsanzo: Ndinapita kumudzi kuti ndikagule chimanga, koma ndayenda mahala. Yenda moyera: Kusavutika kwenikweni ukamachita zinthu. Chitsanzo: Mukuyenda moyera chifukwa ine ndinakhetsa thukuta. Yenda ndi msana: Kunyada kosasamala nako za ena. Chitsanzo: Kodi munthu ukalemera ndiye uyambe kuyenda ndi msana? Yenda pamtsetse: Mawuwa amanenedwa zinthu zikamayendera munthu wina. Chitsanzo: Masiku ano akuyenda pamtsetse. Yenda paphazi: Kudana ndi munthu. Chitsanzo: (1) Anyamata aja ayamba kuyendana paphazi. (2) Anthu amene ndimakhala nawo moyandikana nyumba andiyenda paphazi. Yenda utsi uli tsitu: Kuyenda mopusa. Chitsanzo: Ichi ndiye ndi chitsiru, chimangoyenda utsi uli tsitu. Yenda zochizochi: Yenda mwamanyazi. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani masiku ano akumayenda zochizochi? 391