Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 391

Paphata pa Chichewa Yang’ana nkhope: Kuchitira kanthu poyang’ana kuti uyu ndi ndani. Chitsanzo: Amfumu akamagawa makuponi akumayang’ana nkhope. Yang’anitsa kutali: Chenjeretsa. Chitsanzo: Anzawo anawayang’anitsa kutali. Yanika inswa: Kukhala bwino, kukhala momasuka. Chitsanzo: Chigawengacho chitamangidwa, anthu anayamba kuyanika inswa. Yankho lothetsa makani: Yankho loti winayo sanganeneponso kanthu. Chitsanso: Anamupatsa yankho lothetsa makani. Yankhulitsa pambali: Kuchititsa kuti wina ayankhule mosakhala bwino, kupsetsa mtima. Chitsanzo: Akufuna andiyankhulitse pambali kuti akapita kumudziko azikanena kuti ndine woipa. Yanokola: Yafa, yasiya kugwira ntchito. Chitsanzo: Galimoto yanga yanokola. Yatsa moto: Danitsa, yambanitsa. Chitsanzo: Pamudzi panu paja pali munthu wina yemwe akuyatsa moto. Yauma: Yatha, yavuta. Chitsanzo: Akangopanda kubwera ndiye kuti ntchito yake yauma. Yavi: Kungoti mbwee, balalabalala, kukhala mosalongosoka. Chitsanzo: (1) Tsitsi lawo langoti yavi! (2) Tathumulani ulusi wangoti yaviwu. Yedzeka ana: Bala ana okongola Chitsanzo: Banja limene lija linayedzeka anyamata okhaokha. 390