Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 390

Paphata pa Chichewa Yagona padenga: Mvula yachezera kuvumba usiku wonse. Chitsanzo: Mvulayi yagona padenga. Yaka: Kuledzera kwambiri. Chitsanzo: (1) Amakonda kuyankhula chingerezi akayaka. (2) Ndawapeza kumowako atayakiratu. Yakaliyakali: Kumangoyendayenda. Chitsanzo: Anthu osowa zochita ali yakaliyakali m’taunimu. Yala liwiro: Kuthamanga kwambiri. Chitsanzo: Atangomva zoti chimanga chafika, analiyala liwiro. Yala udzu: Pusitsa. Chitsanzo: Sizimasowa munthu akamayala udzu. Yalakwa: Zavuta, ndapalamula. Chitsanzo: Nditangopsereretsa ndiwo ndinadziwa kuti yalakwa. Yamala: Yatha. Chitsanzo: Ntchito yawo yamala. Yamtidzi: Yabwino kwambiri, yawofuwofu. Chitsanzo: Galimoto yake ndi yamtidzi. Yamwa mphamvu: Fooketsa. Chitsanzo: Mwala umenewu wayamwa mphamvu zanga. Yamwirira: (a) Kulowerera. Chitsanzo: Dikirani kuti thonjeli liyamwirire madziwa. (b) Wokhala kapena kubadwa m’banja lomwelo. Chitsanzo: Anthu amene amathandizana amakhala oyamwirira. Yandikiza: Bweretsa pafupi. Chitsanzo: Mukaona kuti sizili bwino, muyandikizitse achinansi onse kuti awauze mawu omaliza. 389