Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 39

Paphata pa Chichewa kupolisi alandira chionamaso. Chipere: (a) Kutha onse. Chitsanzo: (1) Ngoziyo itachitika, onse omwe anali m’basiyo anali chipere. (2) Pamene njalayo inkatha, mudzi wonse unali chipere. (b) Kunyenyeka. Chitsanzo: Munthu wina anagundidwa ndi sitima moti anthu anangopeza chipere. (c) Ndiwo zopangidwa ndi nyemba, khobwe kapena nandolo. Nthawi zambiri amanyenya zinthuzi n’kukhala ngati phala. Chitsanzo: Lero tidyera chipere. Chiphadzuwa: Mkazi wokongola kwambiri. Popeza dzuwa limawala kwambiri komanso palibe munthu amene anganene kuti sakuliona likamawala, mkazi wokongola sasowa komanso aliyense amadziwa kuti pali munthu apa. Chitsanzo: Ana a a Bengo ndi ziphadzuwa zokhazokha. Chiphala: Munthu wopusa ndi wosadziwa kanthu. Chitsanzo: Mnyamata uyu ndi chiphala. Chiphamaso: Kuchita zinthu mwachinyengo. Chitsanzo: Mumpingo mwanumu mwadzadza anthu achiphamaso. Chiphapha: (a) Munthu wopanda mphamvu. Chitsanzo: Sanganimenye ine. Iye ujatu ndi chiphapha. (b) Chigalimoto kapena chipangizo china chakutha. 38