Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 388

Paphata pa Chichewa Wototobwa: Wopusa. Chitsanzo: Bambowa ndi wototobwa. Wotukwanitsa mafupa: Mwana waulesi, mwana wopanda khalidwe. Chitsanzo: Iwe ndiwe mwana wotukwanitsa mafupa. Wouma m’maso: Munthu wosalira nsanga. Chitsanzo: Mwanayu ndi wouma m’maso, ngakhale umumenye salira. Wouma mtima: Wopanda chisoni, wosamva chisoni. Chitsanzo: (1) Mtsikanayu ndi wouma mtima. (2) Anthu ambiri ogwira ntchito kumotchale amakhala ouma mtima. Wouma mutu: Wopanda nzeru. Chitsanzo: Mwanayu ndi wouma mutu, m’kope mwake muli zithetho zokhazokha. Wowala: Wokongola. Chitsanzo: Komatu mtsikana uja ndi wowala! Wowirira: Wovuta. Chitsanzo: (1) Aphunzitsi athu ndi wowirira, safuna zachibwana. (2) Mayeso anatilembetsa lero anali owirira. Woyamwa lina: Munthu wadera yemwe si m’bale wako. Chitsanzo: Uzithandiza abale ako m’malo mothandiza woyamwa lina. Woyangata ena: Wachisoni, wokonda kuthandiza ena. Chitsanzo: Amalume ndi munthu woyangata ena. Woyendayenda: Wokonda chiwerewere. Chitsanzo: Azimayi oyendayenda amakhala opanda manyazi. Wozerezeka: Wamisala, wosaganiza bwino. Chitsanzo: Chimenechi si chikondi ayi, wina wazerezeka. Wozezeduka: Wochenjeretsa, wotengeka. Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi wozezeduka. 387