Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 387
Paphata pa Chichewa
Wosokonekera: Wopanda khalidwe.
Chitsanzo: Ali ndi mwana m’modzi yekha koma ndi
wosokonekera.
Wosunga malamulo: Womvera malamulo.
Chitsanzo: Pasukulu pano tikufuna ana osunga
malamulo.
Wosunga pakamwa: Wosakonda kuyankhula nkhani
zachinsinsi.
Chitsanzo: Mwana ameneyu ndimamukhulupirira, ndi
wosunga pakamwa.
Wosweka mutu: Wolongolola, wovuta.
Chitsanzo: Atsikana ambiri amakhala osweka mitu.
Wotakata: Wachimasomaso.
Chitsanzo: Ndamva kuti ukuyenda ndi mtsikana wotakata
uja, samala utenga zosatenga.
Wothetsana: Kukangana kwambiri.
Chitsanzo: Ankhonswe anatopa nawo, amangokhalira
kuothetsana nthawi zonse.
Wothirathira thendo kale: Mtsikana wamkulu, mtsikana
wotha msinkhu, mbeta.
Chitsanzo: Kunyumbaku kuli wothirathira thendo kale.
Wotisonkhera moto: Mtsikana wosakwatiwa kapena kuti
mbeta.
Chitsanzo: Tabwera kwanu kuno kuti tidzapeze
wotisonkhera moto.
Wotopa ndi mphasa: Munthu yemwe wadwala kwa
nthawi yaitali.
Chitsanzo: Ndinabwera kuno kudzaona wotopa ndi
mphasa, sindinabwerere maliro.
Wotopa: Mayi amene wangotsala pang’ono kubereka
mwana.
Chitsanzo: (1) Mayi wotopa amakhala wovuta. (2) Akazi
awo ndi wotopa.
386