Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 386

Paphata pa Chichewa (b) Wovuta kwambiri. Chitsanzo: Akanadziwa kuti nanenso ndi wopenga sakanandiputa. Wopeza bwino: Andalama, olemera. Chitsanzo: Banja lawo ndi lopeza bwino. Wopulukira: Wosokonekera, wosaphunzira, kuwonongeka. Chitsanzo: Makolo akamalekerera mwana, mwanayo amapulukira. Wosalongosoka: Wa khalidwe loipa, kawirikawiri amakhala hule. Chitsanzo: Mtsikana mukufuna kumanga naye banjayu ndi wosalongosoka. Wosamva: Munthu amene umati ukamuuza zinthu sachita, kapena kumuuza zina iye kuchita zina. Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi wosamva. Wosanunkha kanthu: Wosathandiza, wopanda ntchito. Chitsanzo: Ife ndiye ndi osanukha kanthu, palibe chimene tingakuthandizeni. Wosanunkha kanthu: Wosathandiza, wopanda ntchito. Chitsanzo: Ife ndiye ndi osanunkha kanthu. Wosasunthika: Munthu wolimba mtima, wamphamvu, wosasinthasintha. Chitsanzo: (1) Amene aja ndi mayi wosatekeseka. (2) Uyu ndi Nkhristu wosatekeseka. Wosatekeseka: (a) Munthu wolimba mtima, wamphamvu, wosasinthasitha komanso wosasunthika. Chitsanzo: (1) Amene aja ndi mayi wosasunthika. (2) Uyu ndi Nkhristu wosasunthika. (b) Kusagwedezeka, munthu wopanda mantha, yemwe sasiya chinthu chifukwa ena akumunyoza. Chitsanzo: Iye samatekeseka ena akamamunyoza. 385