Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 385
Paphata pa Chichewa
Woodzera, wogona, watulo: Wopusa.
Chitsanzo: (1) Koma ndiye mwamuna wake ndi wogonatu.
(2) Kuchikamwini sikufuna munthu woodzera. (3) Zinthu
siziwayendera chifukwa ndi atulo.
Woola pakamwa: Wotukwana kwambiri.
Chitsanzo: Anamasina ndi owola pakamwa.
Woona mtima: Munthu wachilungamo, wopanda
chinyengo.
Chitsanzo: Ntchito ya kubanki imafuna anthu oona
mtima.
Woonekera m’mimba: Mwana wamn’gono.
Chitsanzo: Sindingamalimbane ndi kamwana koonekera
m’mimba ngati kamene kaja.
Woonekera matumbo: Mwana wamng’ono kwambiri.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani bambo akulukulu aja
akuyenda ndi mwana woonekera matumbo uja.
Wopanda khalidwe: Wakhalidwe loipa.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wopanda khalidwe.
Wopanda makutu: Wosamva malangizo a ena.
Chitsanzo: (1) Anafa chifukwa anali wopanda makutu. (2)
Ngakhale mumuyankhule saamva, alibe makutu.
Wopanda ndi khodo yomwe: Wopanda ndalama.
Chitsanzo: Kodi munthu ungadye chikondi ngati
utavomera munthu wopanda ndi khodo yomwe?
Wopanda pake: Wosathandiza, wopanda ntchito.
Chitsanzo: Ameneyu ndi munthu wopanda pake.
Wopata: Andalama, olemera.
Chitsanzo: Bambo awo ndi wopata.
Wopenga:
(a) Wamisala.
Chitsanzo: Openga ena amangoyankhula chizungu
chokhachokha.
384