Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 384
Paphata pa Chichewa
analoleranji mwamuna wakuda chonchija. Nkhani yake
ndi yakuti mwamuna uja ndi wokongola m’nthumba.
Wokulupala: Wojintcha, wonenepa.
Chitsanzo: Mwanayu wayamba kukulupala.
Wolema: Ali pafupi kubala mwana.
Chitsanzo: Mayi anabwerayo ndi wolema.
Wolimba m’maso: Amene sagona nsanga.
Chitsanzo: Mwana uyu ndi wolimba m’maso.
Wolimba moyo: Wopirira, wakhama.
Chitsanzo: Mayiyu ndi wolimba moyo.
Wolozeka:
(a) Wokongola, wosachititsa manyazi.
Chitsanzo: (1) Ali ndi ana olozeka. (2) Ukapeza mkazi
wolozeka anthu amakupatsa ulemu.
(b) Kulemera kapena kukhala ndi chuma.
Chitsanzo: Banja lawo ndi lolozeka.
Wombetsa mitu: Kudanitsa anthu.
Chitsanzo: Ndani amene wawaombanitsa mitu?
Wombetsa nsalu: Kulukitsa nsalu.
Chitsanzo: Ndikufuna ndikawombetse nsalu yokhala ndi
nkhope yanga.
Womva zake zokha: Wosasamala malangizo kapena
maganizo a ena.
Chitsanzo: Mwamuna wako akakhala womva zake zokha
pa nkhani zandalama, umafunika kumangosolola
ndalama ya ndiwo kuti upangeko chitukuko.
Wonekera ng’amba: Kuyaluka, kuonekera poyera.
Chitsanzo: Lero ndiye waonekera ng’amba, anamugwira
akupopa mafuta m’galimoto yamwini.
Wonekera nyangalazi: Kuululika.
Chitsanzo: Mkulu uja waonekera nyangalazi atagwidwa
ali ndi mkazi wa mwini.
383