Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 383

Paphata pa Chichewa Woimba yemwe amadula waya: Waluso kwambiri poimba gitala. Chitsanzo: Nthawi imeneyo oimba amene ankadula waya anali achina Michael Yekha, Tambala Chitenje ndi ena otero. Wojintcha: Wamphamvu. Chitsanzo: Mnyamata wake ndi wojintcha. Wokankha ndege: Munthu wa akatumba aakulu. Chitsanzo: Anzanu ali ndi akatumba ngati wokankha ndege. Wokhwima: (a) Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito akamanena zokhudza zikhulupiriro za ku Africa kuno zokhudza matsenga. Amanena za munthu amene pa nkhani za matsenga komanso ufiti ndi patali. Chitsanzo: Akulu a imvi aja ndi wokhwima. (b) Munthu wamkulu. Chitsanzo: Banja limafuna anthu okhwima. Wokhwimitsa zinthu: Munthu wankhanza, munthu wo- kakamira malamulo. Chitsanzo: Makolo anga ndi okhwimitsa zinthu. Wokodzera khoma: Munthu wamwamuna. Chitsanzo: Anthu ambiri amaopa pakhomo pakakhala okodzera khoma. Wokomoka: Wakugwa khunyu, wamisala. Chitsanzo: (1) Mwanayu amakomoka. (2) Ali ndi mwana wokomoka. Wokonda amuna: Wachiwerewere. Chitsanzo: Atsikana okonda amuna amakhala achikondi. Koma vuto ndi lakuti sasankha munthu womusonyeza chikondicho! Wokongola m’nthumba: Wandalama. Chisanzo: Anthu amakonda kufunsa kuti mayi aja 382