Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 382

Paphata pa Chichewa Woduka mutu: Wopanda mnzeru. Chitsanzo: Sindimadziwa kuti mayiwa ndi woduka mutu! Wodwala m’mutu: Wosokonekera, wovuta. Chitsanzo: Mtsikana ameneyu ndi wodwala m’mutu. Wodwala: (a) Ali ndi mimba. Chitsanzo: Mtsikana wanuyu ndi wodwala. (b) Wamisala, yemwe mutu wake suyenda bwino. Chitsanzo: Bambo uja ndi wodwala. Wodya matako a galu: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Safuna kukhala pansi, amakhala ngati anadya matako a galu. Wodzikhuthula: Wodzipereka. Chitsanzo: (1) Amagwira ntchito modzikhuthula ngati anabadwira zomwezo. (2) Mnyamata ameneyu ndi wodzikhuthura. Wodzilimbikira: Wolimbikira ntchito, wakhama. Chitsanzo: Munthu wodzilimbikira ndi amene amalemera. Wodzipereka: Wakhama, amadzipereka kuchita chilichonse. Chitsanzo: Mnyamatayu ndi wodzipereka pantchito. Wofunda nthunzi: Wopusa. Chitsanzo: Achimwene anu aja ndi wofunda nthunzi. Wogangalama: Wovuta. Chitsanzo: Bambo uja ndi wogangalama. Wogona, watulo, wozizira, wodontha, wochucha: Munthu wopusa. Chitsanzo: Ukhoza kumupusitsa, munthu wake ndi wogona. Wogunata: Wopusa. Chitsanzo: Ukamayenda ndi munthu wogunata, nawenso umasanduka wogunata. 381