Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 381

Paphata pa Chichewa Wirawira: Lendelende, kulendewera. Chitsanzo: Agogo awo akamayenda amangoti nsanza wirawira. Wiringula: Dandaula, nyinyirika. Chitsanzo: Anthu akumangowiringula, akuti chimangachi chikudula. Wobaizika: Wamisala. Chitsanzo: Kubanja lawo kuli anthu ambiri obaizika. Wobalalika: Munthu yemwe zimakonda kumusokonekera. Chitsanzo: Achimwene anu aja ndi wobalalika, ukawauza kuti achite chinthu amangoti maso mwazumwazu. Wobwebweta: (a) Wogwidwa ndi mizimu. Anthu ena amakhulupirira kuti mizimu imatha kuthandiza anthu kudziwa zam’tsogolo. Chitsanzo: Kumtundaku kuli mayi wobwebweta, akhoza kukuuzani chifukwa chake mukukumana ndi mavuto. (b) Munthu amene amayankhula akamagona. Chitsanzo: Akaona zoopsa amabwebweta akamagona. Wobwevuka: Wolongolola. Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi wobwevuka. Wocha pakamwa: Wodziwa kuyankhula. Chitsanzo: Kwa amfumuko mutumizeko munthu wocha pakamwa. Wochenjera pakamwa: Wodziwa kuyankhula. Chitsanzo: Mwanayu ndi wochenjera pakamwa. Wochita zinthu mwaumoyo: Mwachibadwa. Chitsanzo: Munthu wodziwa kuyankhula amachita zinthu mwaumoyo. Wochuluka nzeru: Wodziona kuti ndi wozindikira. Chitsanzo: Achimwene ndinu wochuluka nzeru kwabasi! Wodikirira matenda: Munthu wodwazika matenda. Chitsanzo: Ndikupita kukadikirira matenda. 380