Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 380

Paphata pa Chichewa (b) Chosalimba. Chitsanzo: Nsungwizi ndi za wedewede. Wedewede: Kupanda mphamvu, kusalimba. Chitsanzo: Ntchito iyi sifuna munthu wawedewede. Wefuwefu: Kupuma mosonyeza kutopa. Chitsanzo: Wathamanga kwa nthawi yaitali moti ali wefuwefu. Wenderera: Yenda mozemberera munthu winawake. Chitsanzo: Eti kubwerabweraku akuwenderera kamkazi kaja! Wengana: Dana. Chitsanzo: Simukudabwa kuti anasiya kuyankhulana. Anawenganatu! Werenga kalata wam’thumba: Kumangoganizira kuti ndi zimene zitachitike. Chitsanzo: Wadziwa bwanji kuti akutenga? Ukuwerengeratu kalata wam’thumba iwe! Werengera madzi amphutsi: Kudikira popanda kanthu, kudalira zinthu zomwe kulibe. Chitsanzo: Ngati ukuganiza kuti ndidzakukongoza ndalama ndiye ukuwerengera madzi amphutsi. Werengera: Kukudalira, kuikidwa m’gulu la anthu ofunika. Chitsanzo: Lero mpamene ndadziwa kuti amandiwerengera kuti ndine m’bale wawo. Werewere: Kuyenda mosadziwika bwino. Chitsanzo: Kodi bambo ameneyu watani akumangoti werewere? Wereweta: Kulongolola, kunena mabodza. Chitsanzo: Uzingowayang’ana akayamba kuwereweta. Wezuka: Kuyera. Chitsanzo: Tiyambe kudzola zodzoladzola kuti nafenso tiwezukeko. 379