Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 38
Paphata pa Chichewa
kwa mwana? Tikuthandizeni kapena kuti mkazi wanuyu
akhale ndi chinja.
Chinunkhira: Kusafuna zinthu chifukwa choti zakukwa-
na. Ngati munthu ali ndi chinunkhira ndi zinazake ama-
khala kuti akuzifuna.
Chitsanzo: (1) Chakudyachi ndilibe nacho chinunkhira.
(2) Maungu ndili nawo chinunkhira.
Chinyanja: Amatanthauza zoyankhula, zonena kapena
mawu.
Chitsanzo: Atamugwira, anasoweratu chinyanja choti
anene.
Chinyezi:
(a) Mwayi.
Chitsanzo: Pakhomo pamene paja pakuoneka kuti pali
chinyezi.
(b) Zambiri.
Chitsanzo: Anthu oyenda pansi anali chinyezi.
Chinyomphiro: Mawu omwe kwenikweni amatanthauza
chakumbuyo cha nkhuku, thako la nkhuku. Koma
amagwiritsidwa ntchito mwachining’a potanthauza mbuyo
ya munthu, thako.
Chitsanzo: Koma mtsikana uja ali ndi chinyomphiro!
Chionamaso: Ndalama imene munthu amalandira
akaona chinachake kapena akatola chinthu.
Chitsanzo: Amene atatole laisesiyo alandira chionamaso.
Chionamaso: Ndalama imene munthu amapatsidwa
akapeza chinthu chimene chimafunidwa.
Chitsanzo: Amene atole chikwamacho n’kukachipereka
37