Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 379

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ana osasamba asatitsatire tikamapita kokawaula mavu. Waula: Kukuuza zabodza. Chitsanzo: Aphunzitsi athu angotiwaulawaula n’kutuluka m’kalasi. Wautali: Ulendo, kunyamuka. Chitsanzo: Ndikangodya nsima ukhala wautali. Wawa: Mawu aulemu omwe anthu amanena akamadutsa pamene pali anthu. Nthawi zina mawuwa angatanthauze chinthu chowawa. Chitsanzo: Wawatu wawa! Tikudutsa nawo. Wazake: Munthu wamisala. Chitsanzo: Mwana woyamba wa mayiwa ndi wazake. Akakhala amangoti tondovilo. Wazala zazitali: Wakuba. Chitsanzo: Azimayi ena ndi azala zazitali. Wazintchito: Wolimbikira kugwira ntchito. Chitsanzo: (1) Timafuna mkazi wazintchito! (2) Mkazi mwamukanayutu ndi wazintchito! Waziwalam’maso: Wamisala. Chitsanzo: (1) Anthu amaganiza kuti ku Lower Shire kuli anthu ambiri aziwalam’maso chifukwa cha kutentha. (2) Masiku ano akumachita zinthu ngati munthu waziwalam’maso. Wazwee: Wamisala. Chitsanzo: Anaputa wazwee, wawakandira galimoto yonse ndi nsomali. Wedewede: (a) Wopanda mphamvu. Chitsanzo: Ganyu yosenza matumba sifuna munthu wa wedewede. 378