Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 378
Paphata pa Chichewa
Waphula: Walemera.
Chitsanzo: Anzanu aja anaphula.
Waphunzo: Wamwano.
Chitsanzo: Mtsikanayu ndi waphunzo, pamamwa pake
pamangobulika mwano wokhawokha.
Waponda mwala: Ali ndi podalira.
Chitsanzo: Akuyankha mwamakani bwanji, mwinatu wap-
onda mwala.
Wapsa katope: Chenjerani kapena nthawi yatha.
Chitsanzo: Wapsa katope, tiyeni tiyambepo kusosa.
Wapsa phwetekere: Chenjerani.
Chitsanzo: Wapsa phwetekere, wina asakuyeretseni
m’maso.
Wapsa ulendo: Ulendo watheka.
Chitsanzo: Wapsa ulendo, ndinyamuka lero!
Wapsa: Ali mmaluzi.
Chitsanzo: Munthu uja wapsa, alibe kalikonse.
Wathupi lakanyenya: Wonenepa. Amanenedwa
poganizira kuti nyama zonenepa ndi zimene zimakhala
bwino kuzipanga kanyenya.
Chitsanzo: Musamalere ana ndi wailesi ya kanema,
zimapangitsa kuti akhale ndi thupi lakanyenya.
Watola chikwama: Walemera.
Chitsanzo: Mwana uja watola chikwama.
Watumidwa: Mawuwa amanenedwa winawake
akamadabwa ndi zochita za munthu wina yemwe
akuoneka kuti akufuna kumulakwitsa kapena kumutapa
m’kamwa.
Chitsanzo: Kodi ukundifunsiranji zimenezi? Watumidwa
eti?
Waula mavu: Kuwotcha chimanga (ena amati mondokwa
kapena dowe).
377