Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 377

Paphata pa Chichewa Wanjatidwa: Wamangidwa. Chitsanzo: Wakuba uja wanjatidwa. Wankhalwe: Wankhanza. Chitsanzo: Mkaziyu ndi wankhalwe. Wansangala: Munthu wosangalala, Mawu akuti mwansangala angatanthauze kulandira munthu bwino. Chitsanzo: Akazi awo ndi ansangalala. (2) Anawalandira mwansangala. Wanyape: Wosafuna kukambirana koma kumangomenyana basi kuti zithepo. Chitsanzo: Mnyamata wachibwibwi uja ndi wanyape, ukamamuuza zachibwana amangoyamba kukuphaphalitsa nawo makofi. Wanyimbo: Munthu wokondedwa kwambiri, mnzako wapamtima. Chitsanzo: Anakumana ndi mnzake wanyimbo. Wapakamwa pakuthwa: Wochenjera pakamwa, wamabodza. Chitsanzo: Chenjera nayeni, ali ndi pakamwa pakuthwa. Wapakamwa: Wolongolola kwambiri. Chitsanzo: Mkazi akakhala wapakamwa, mwamuna amayamba kukonda bawo. Wapala: Walephera. Chitsanzo: (1) Amakonda kujomba ndiye wapala. (2) Amene wakhoza ndi uyu, mnzakeyo wapala. Wapamtima: Wokondedwa kwambiri. Chitsanzo: (1) Ameneyu ndi mwana wawo wapamtima. (2) Alibe bwenzi lapamtima. Wapezeka: Wadwala kwambiri, wavutika. Chitsanzo: Komatu m’bale wathuyu wapezeka! Wapha ulusi: Wavala bwino. Chitsanzo: Koma ndiye mwauphatu ulusi, mukupita kuti? 376