Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 374

Paphata pa Chichewa Wafukizi: Munthu wovuta. Chitsanzo: Mwana wafukizi sangakhale pano, ndikhoza kumupha. Waimba yakale: Kuchita zothaitha, kuchedwa. Chitsanzo: Inutu mukuimba yakale. Zinthu mukufunazo zinatha kalekale. Wakucha: (a) Wochenjera. Chitsanzo: Ana ambiri akumacha mofulumira masiku ano. (b) Wamkulu woti akhoza kukwatira kapena kukwatiwa. Chitsanzo: Pakhomo pawo pali atsikana angapo akucha. Wakula watha: Mawuwa angatanthauze kuti ndi munthu wamkulu aziona. Chitsanzo: Musiyeni ndi wamkulu ameneyu, wakula watha! Wakunjira: Munthu wobwera. Chitsanzo: Akunjira, takulandirani! Koma musanakhale pansi, tiyeni tikakulozereni pamene panagona m’bale wathu. Walemba m’madzi: Walephera. Chitsanzo: Ngati umaganiza kuti undipusitsa, walemba m’madzi! Walisha n’ngwakhungu: Wosazindikira. Chitsanzo: Koma iye uja sadziwa kuti zinthu zimenezi n’zodula? Musiyeni, walisha n’ngwakhungu. Walobodolobodo: Wofooka. Chitsanzo: Ulimi sumafuna munthu walobodolobodo. Wam’kamwa moola: Wotukwana. Chitsanzo: Atsikana ambiri amakhala am’kamwa moola. Wam’kamwa: Wolongolola. Chitsanzo: (1) Azimayi onse a pamudzi paja ndi am’kam- wa. 373