Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 371

Paphata pa Chichewa Vulira malaya: Kukonzekera kugwira ntchito, kutsimikiza kuti ntchito ilipo. Chitsanzo: Anawaphikira nsima yangati phiri, ndipo anachita kuivulira malaya n’kuyamba kuichita kanthu. Vumata: Kuika m’kamwa koma osameza kapena kuluma. Chitsanzo: Azimayi amavumata phala asanadyetse mwana wawo. Vumbuluka: Kubwerera kumudzi patapita nthawi yaitali, kubwera mwadzidzidzi. Chitsanzo: Chakuchititsani n’chiyani kuti muvumbuluke kutauniku? Vumbulutsa: Thamangitsa, thotha, sokoloka. Chitsanzo: Akakupezani pamenepa akuvumbulutsani. Vumbwa: (a) Chita manyazi, nyowa ndi mvula. Chitsanzo: Anayankhula zoduka mutu, moti anavumbwa kwabasi. (b) Onse omwe anayenda wapansi avumbwa. Vundula: Yambanditsa anthu, danitsa, ononga zinthu. Chitsanzo: Wachoka atavundula pamudzi pano. Vuvuta: Kumenya munthu koopsa. Chitsanzo: Amuvuvuta anzake. Vwivwiniza: Kukhulitsa, kugwetsera chinthu penapake. Chitsanzo: Anamugwira n’kukamuvwivwiniza m’madothi. 370