Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 37

Paphata pa Chichewa (b) Osadziwa kanthu. Chitsanzo: Si bwino kumapita ku mlandu chimutumutu. Chimwanamayi: Ndi mwambo umene anthu a zikhalidwe zina amagwirizana kuti asinthane akazi awo. Zimakonda kuchitika pakati pa mabwenzi apamtima ndipo zimene amachitazi zimakhala ngati abwerekana akazi. Chitsanzo: Malinga ndi muliri wavutawu, ndi chibwana kumachitabe chimwanamayi. Chimwitsa: Kupereka mimba. Chitsanzo: Mnyamatayu ndi amene wachimwitsa mwana wa Abengo. Chinameta nkhanga mpala: Zoopsa. Chitsanzo: Ananena kuti akuonetsani chinameta nkhanga mpala. Chinasala: Chisilamu. Chitsanzo: Sadya nkhumba chifukwa ndi a chinasala. Chindapusa: Zimene munthu amalipira akapalamula. Chitsanzo: Amfumu akanena kuti ulipire chindapusa cha nkhuku ziwiri, inayo amatenga n’kukamwera mowa. Ching’onga: Munthu wamantha. Nthawi zambiri, mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ndi munthu amene wakwiya ndipo akunena mnzake kuti ndi wamantha. Chitsanzo: Iwe ndiwe ching’onga ndithu, khwangwala wachabechabe. Chinja: Mawuwa amatanthauza pakati, pathupi ndipo ena amati mimba. Mawu amenewa amanenedwa mkazi akatenga pakati. Mwachitsanzo: Kodi zaka zizingodutsabe tisanamve kulira 36