Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 369

Paphata pa Chichewa (b) Utsi wamoto. Chitsanzo: Utsi sufuka popanda moto. Utyupi: Woneneza ena kuti iyeyo akome. Chitsanzo: Anthu ena amapita kwa amfumu n’kukachita utyupi kuti akome. Uwa: Yankhula. Chitsanzo: Ndani amene akuuwa panjayo, sakudziwa kuti anthu akugona m’nyumba muno? Uzira: (a) Kupemerera. Chitsanzo: Tauzirani pamotopo kuti uyake. (b) Kuuza munthu zoti achite kapena alembe. Chitsanzo: Mwanayu anzake anamuuzira mayeso. 368