Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 368

Paphata pa Chichewa Unyopo (unyopi): Ulesi. Chitsanzo: Unyopo umachititsa kuti pakhomo padutse galu wakuda. Uone kolowera: Uone kopita. Chitsanzo: Ngati susesa m’nyumbamu uone kolowera, sin- difuna ana aulesi pakhomo pano! Uphungu: Malangizo. Chitsanzo: M’pofunika kuti mwana wanuyu mumupatse uphungu. Upo: Msonkhano wokumana kuti muthandizane nzeru. Chitsanzo: Ayambapo kupanga upo. Usade nkhawa: Usavutike maganizo, usataye mtima. Chitsanzo: Usade nkhawa, ndikuthandiza. Usamangokhala nsidze zili tsende: Uziyendayendako. Chitsanzo: Osamangokhala nsidze zili tsede, kumawongolako miyendo. Usatitsegule m’mimba! Usativutitse, usatinyanse. Chitsanzo: Nanunso mukufuna mutitsegule m’mimba ndi kamkonono ka wailesi mwagulayo. Usodzi wolula: Usodzi woti ukapita kosodza subwerako chimanjamanja. Chitsanzo: Anzathu amachita usodzi wolula. Utakafumbi: Mbewa. Chitsanzo: Lero tidyera utakafumbi. Utchisi: Uve. Chitsanzo: Anthu a pakhomo pano ndi a utchisi. Utsa mapiri pachigwa: Kuchititsa kuti anthu adane kapena ayambane. Chitsanzo: Osamachita zinthu zoutsa mapiri pachigwa. Utsi: (a) Munthu wopusa. Chitsanzo: Ntchito ngati imeneyi sifuna munthu wa utsi. 367