Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 366

Paphata pa Chichewa Ululu: Kuwawa, kupweteka. Chitsanzo: Ndikumva ululu woopsa. Uma manja: Woumira. Chitsanzo: Mukapanda kuphunzitsa anawa kukhala owolowa manja, adzakhala ouma manja. Uma mutu: Kupanda nzeru, kusamva. Chitsanzo: (1) Sakhoza m’kalasi chifukwa ndi wouma mu- tu. (2) Ana anu onse ndi ouma mitu. Uma pakamwa: Chita mantha kuulula. Chitsanzo: Ndimafuna ndikuuzeni zinazake koma ndangouma pakamwa. Uma: (a) Leka kubereka. Chitsanzo: Akazi awo aja ndi wouma. (b) Kutha Chitsanzo: (1) Ntchito yawo yauma. (2) Katungeni madzi kumjigo chifukwa mtsuko wauma. Umandiyesa kape? Undiyesa chitsiru? Chitsanzo: N’chifukwa chiyani ukundiyang’ana choncho? Umandiyesa kape eti? Umbanda: Kuba, chifwamba. Chitsanzo: Boma lalonjeza kuti lithetsa umbanda. Umbombo: Kumana. Chitsanzo: Mwanayu ndi waumbombo. Umbudza: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Galu wakubayu ndi wofunika kumuumbudza. Umphawi: Usiwa, kusowa, kusauka. Chitsanzo: Ali pa umphawi wadzaoneni. Undisamale! Chenjera nane. Chitsanzo: Undisamale, ndikhoza kukumenya! Undwa: Kungodikira pachabe, kupusitsidwa. Chitsanzo: (1) Zikanakhala zayenda simukanandipeza 365