Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 364
Paphata pa Chichewa
Ubwana:
(a) Kukhala mwana.
Chitsanzo: Ankabwera kuno ali pa ubwana wake.
(b) Kukhala bwana.
Chitsanzo: Masiku ano anayamba kudziona ubwana, moti
kuno sabwera.
Ubwenzi wonyambitana: Chikondi champhamvu kwam-
biri.
Chitsanzo: Anyamatawa ali pa ubwenzi wonyambitana.
Uchitsiru: Kupusa, kupanda nzeru.
Chitsanzo: Chitsiru ngakhale mutachisinja mumtondo,
uchitsiru wakeyo sungamuchoke.
Ufupiufupi: Zovala zimene atsikana komanso anyamata
amakono akumavala zomwe zikumakhala zifupizifupi
kapena zothina kwambiri.
Chitsanzo: Ndimachita manyazi ndikamayankhula ndi
mtsikana atavala ufupiufupi.
Ugogodi: Kuneneza wina miseche.
Chitsanzo: Mukapitiriza kuchita ugogodi akuthamangi-
tsani māmudzi muno.
Uhule: Kugonana ndi anthu ena kuti akupatse ndalama.
Limeneli ndi dzina la sipanala ina ya njinga, yomwe ima-
khala ndi mabowo ambirimbiri. Sipanalayi ukhoza kukon-
zera njinga yamtundu ulionse.
Chitsanzo: Mtsikana akayamba kuyenda usiku, amakhala
kuti wayamba uhule.
Ukachenjede: Luso lapadera kwambiri. Munthu amene
ali ndi luso limeneli amamutchula kuti kachenjede.
Chitsanzo: (1) Ndikufuna kukachita maphunziro a
ukachenjede. (2) Ndinakumana ndi kachenjede wama-
samu.
363