Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 363
Paphata pa Chichewa
Tula mtolo: Uza munthu wina mavuto ako kuti
akuthandize.
Chitsanzo: Ndawatulira mtolo wanga.
Tulo tofanato: Tulo tatikulu.
Chitsanzo: Ndikalawako pang’ono m’pamene ndimagona
tulo tofanato.
Tulo: Kupusa.
Chitsanzo: (1) Sindifuna kudzakwatiwa ndi mnyamata
watulo. (2) Akuba amachenjeretsa anthu atulo.
Tuluka m’nyumba: Kusiya mwamuna kapena mkazi
wako n’kumakagona ndi ena.
Chitsanzo: Mayi awa amatuluka m’nyumba
n’kumakakumana ndi amuna ena.
Tumbula: Nena mfundo yeniyeni.
Chitsanzo: Musamazungulire, tangotumbulani!
Tumbwa: Nyada.
Chitsanzo: Akakhala nazo amatumbwa kwabasi.
Tunga mowa: Kuledzera kwambiri.
Chitsanzo: Akuoneka kuti autunga mowa.
Tunguluza: Mmene munthu amaonekera akamayendetsa
maso ndi zikope ponyoza wina kapena posonyeza kuti
sakugwirizana ndi zomwe wina akunena kapena kuchita.
Chitsanzo: Ambiri anayamba kutunguluza maso atamva
mbwerera zimene amanenazo.
Tunthumira: Kuchita phuma kapena mantha, kufuni-
tsitsa chinachake.
Chitanzo: (1) Akutunthumira ndi mantha. (2) Usamachite
kutunthumira, akupatsa.
Tuzula maso: Tulutsa maso pamtunda.
Chitsanzo: Ndinawaona akukutuzulirana maso, n’kutheka
anauzana zinazake.
362