Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 361
Paphata pa Chichewa
Tsitsa mfundo: Kunena zinthu zanzeru.
Chitsanzo: Mwanayu amatsitsa mfundo.
Tsitsi bi!: Ali khale.
Chitsanzo: “Kodi mnyamata anasiya ntchito uja akutani?”
“Ali tsitsi bi kunyumbaku.”
Tsitsimuka: Kumva bwino, kusangalala.
Chitsanzo: (1) Mawu a Mulungu amanditsitsimula. (2)
Ndipite kunyanja ndikatsitsimuke n’kukamiza nkhawa
zanga.
Tsitsitiza: Maliziratu zonse.
Chitsanzo: Matendawo anatsitsitiza anthu onse.
Tsogola: Mwalira.
Chitsanzo: Achimwene aakulu aja ndi amene anatsogola.
Tsokaliyenda: Munthu amene amangokumana ndi
mavuto.
Chitsanzo: Kodi mwakumana ndi tsokaliyenda.
Tsopa mowa: Kumwa mowa wambiri.
Chitsanzo: Bambo ake amautsopa mowa.
Tsuka m’kamwa: Kudya chakudya chankhuli.
Chitsanzo: (1) Tisungire ndalama kuti tidzatsuke m’kam-
wa pa nyuwere. (2) Tiphe kalulu kuti titsukeko m’kamwa.
Tsuka maso (m’maso):
(a) Onera filimu, masewera enaake kapena kuona
chinachake chosangalatsa.
Chitsanzo: (1) Lero kuli mpira wa Buletsi ndi Manoma,
ndipita kuti ndikatsuke m’maso. (2) Tiloweko m’tauni
tikatsuke maso.
(b) Kusukusula.
Chitsanzo: Apatseni madzi kuti atsuke m’maso.
Tsukuluza: Lalatira, tukwana, nyoza munthu.
Chitsanzo: Si bwino kumayambana ndi munthu amene
uja chifukwa akhoza kukutsukuluzani.
360