Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 360
Paphata pa Chichewa
Tsina ndi therere: Kupanda mphamvu.
Chitsanzo: Gwira mwamphamvu, osamakhala ngati
anakutsina ndi therere.
Tsinana makutu: Kuuzana zinazake zachinsinsi,
kuchenjezana.
Chitsanzo: (1) Bwerani titsinane makutu. (2) Tikaona zoda-
bwitsa tizitsinana makutu.
Tsindwi limalimba ndi mnzati: Munthu akakhala pa-
mavuto amamuthandiza ndi mnzake.
Chitsanzo: Tizithandizana, tsindwi limalimba ndi mnzati.
Tsindwi: Denga.
Chitsanzo: Mwaye umapezeka kutsidwi ngati mumaphiki-
ra m’nyumba.
Tsinira mafulufute kuuna: Kutsekereza zabwino.
Chitsanzo: Apatu ndiye mwatsinira mafulufute kuuna,
sadzakupatsaninso ina.
Tsintho: Kusinthana zinthu, wina kutenga china wina
chanzake.
Chitsanzo: Tiyeni tingopanga tsintho.
Tsinzinan’tole: Munthu wakuba, mbala.
Chitsanzo: (1) Kuti atsinzinamtole asakubere, umafunika
kusunga ndalama zako mosamala. (2) Anthu akagwira
tsinzina n’tole, akumangomupatsa gwanda kapena shati.
(3) Samalani, m’tauni muno mwachuluka a tsinzinan’tole.
Tsira diso: Kupita kukaona munthu kapena chinthu.
Chitsanzo: (1) Mungandibwerekeko bukulo kuti
ndilitsireko diso. (2) Ndinaona kuti ndisangobwerera
ndisanakutsireni diso.
Tsira mphepo: Kalipira kwambiri.
Chitsanzo: Akamafuna kuyamikira munthu amayamba
kaye amutsira mphepo.
359