Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 36
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Zoona mungabwere kuno chimanjamanja.
(2) Osamapita kwa amfumu chimanjamanja.
Chimasomaso: Uhule kapena kuchita chiwerewere.
Chitsanzo: Azimayi ambiri a m’mudzi uwu ndi
achimasomaso.
Chimbalangondo: Munthu woipa mtima, wovuta.
Chitsanzo: Pamene ankabwera kuchokera kundende anali
atasanduka chimbalangondo.
Chimbayambaya: Munthu wosalongosoka, munthu
wopanda khalidwe.
Chitsanzo: Mkazi akufuna kumanga naye banja uja ndi
chimbayambaya.
Chimkukuluzi: Njala ya dziko lonse. Timagwiritsa ntchito
mawu amenewa tikamanena za njala yomwe sinasiye
khomo.
Chitsanzo: Kuvuta kwa mvulayi ndi chizindikiro choti
chaka chino kukhala chimkukuluzi.
Chimphona: Munthu wamphamvu kwambiri. Nthawi
zambiri amakhalanso wandewu.
Chitsanzo: Ndani angalimbane ndi chimphona ngati
chimene chija!
Chimunthu:
(a) Anthu ambiri.
Chitsanzo: Kumsonkhanoko kunali chimunthu.
(2) Mpeni wosathwa kapena wobuntha.
Chitsanzo: Mpeni wapakhomo pano ndi chimunthu.
Chimutumutu:
(a) Kuyenda osasenza kanthu.
Chitsanzo: Mayiyo anati: “Ifetu tangobwera chimutumutu.”
35