Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 359
Paphata pa Chichewa
Tsembwe (tsemwe): Kuchita mantha kapena manyazi.
Nthawi zina munthu ukamachita mantha pakhungu
pamatuluka timadontho tinatake, timeneto ndiye tsembwe
(tsemwe).
Chitsanzo: Nditangoona kuti amubaya, thupi langa lonse
linachita tsembwe.
Tsengera: Sintha mawu.
Chitsanzo: Atamupanikiza, anayamba kutsengera.
Tsetsera: Mwalira.
Chitsanzo: Sindimadandaula munthu woipa akatsetsera.
Tsika:
(a) Vina mwaluso.
Chitsanzo: Mtsikana uja akati atsike, simungamukonde.
(b) Munthu amene amadwala akatsirizika.
Chitsanzo: Munthu timanena kuti wadwala kwa nthawi
yaitali uja akuti watsika tsopano.
Tsilira mang’ombe: Kuwonjezera zina kuti nkhani ikome,
kupokolezana nyimbo.
Chitsanzo: (1) Ndati nditsirirepo mang’ombe za munthu
mwatamulayo. (2) Pamene ena amaimba, ena amatsirira
mang’ombe.
Tsilira mavume: Kuwonjezera zina kuti nkhani ikome,
kupokolezana nyimbo.
Chitsanzo: (1) Ndati nditsirirepo mavume za munthu mwa-
tamulayo. (2) Pamene ena amaimba, ena amatsirira
mavume.
Tsina khutu: Kuululira munthu zinazake.
Chitsanzo: (1) Bwerani pang’ono ndikutsineni khutu za
munthu akubwerayo. (2) Mwamva zimene zachitika
kumtundaku? Tabwerani kuno ndikutsineni khutu!
358