Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 358
Paphata pa Chichewa
Tsakamuka:
(a) Kugwa modetsa nkhawa.
Chitsanzo: Anatsakamuka mumtengo wamango.
(b) Kuchoka paudindo.
Chitsanzo: Anatsakamuka paudindo wawo.
Tsala madzi amodzi: Kutsala pang’ono kufa kapena
kutha.
Chitsanzo: (1) Ndinadwala kwambiri moti ndinangotsala
madzi amodzi. (2) Nyembazi zangotsala madzi amodzi.
Tsala:
(a) Malo osalimidwa.
Chitsanzo: Anapha njoka pa tsala lija.
(b) Kuuza munthu kuti asakutsatire.
Chitsanzo: Tsala, kunjaku kwada.
Tsamira mkono (gonera dzanja): Mwalira.
Chitsanzo: (1) N’zachisoni kuti bambo aja atsamira mkono.
(2) Mudzandilira ndikadzagonera dzanja.
Tsanura: Kupungula.
Chitsanzo: Titsanunireni mafutawo.
Tsatanetsatane: Molongosoka, motsatira dongosolo lake.
Chitsanzo: Tafotokozani mwatsatanetsatane.
Tsekera mbewa kuuna: Tsekereza zokoma.
Chitsanzo: Anthu amafuna kukuthandizani inu
n’kuwaberanso! Mwatsekereza mbewa kuunatu pame-
nepa!
Tsekera:
(a) Pumira kaye, maliza kuti udzayambenso nthawi ina.
Chitsanzo: Ana atsekera sukulu.
(b) Udzu wokhwima bwino.
Chitsanzo: Akukadula tsekera.
Tseketseke: Kumva bwino, kukoma, kuzuna,
kutsekemera.
Chitsanzo: Mzimbeyi ili tseketseke.
357