Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 356
Paphata pa Chichewa
Tibula: Kumenyedwa kwambiri.
Chitsanzo: Akachita masewera ndimutibula.
Tichedwepo: Tikambirane bwinobwino, tionetsetsepo
bwinobwino.
Chitsanzo: Koma pa nkhani iyi yokha tichedwepo.
Tigwira mtengo wanji? Mawuwa amanenedwa munthu
akamadandaula kuti achita bwanji, kapena akathedwa
nzeru n’kumasowa chochita.
Chitsanzo: Njala imeneyi kaya tigwira mtengo wanji!
Tigwire mtengo wanji? Titani, tichite chiyani?
Chitsanzo: Ndalema nazo, kaya ndigwire mtengo wanji?
Timere mizu: Kukhazikika.
Chitsanzo: Mkamwini ameneyu wamerapo mizu pakhomo
pano.
Titere: Mawuwa amayankhulidwa munthu akamapereka
chinachake, chinthu kapena moni.
Chitsanzo: Panja ndinabwereka ndalama zanu eti? Ndiye
titeretu! (2) Tiwapatse kaye moni athuwa! Titeretu!
Titimira: Lowa m’matope, kanirira.
Chitsanzo: Galimotoyo imangovinavina m’matope, kenako
inatitimira.
Tiuzeni pamene mwaima! Tiuzeni maganizo anu.
Chitsanzo: Popeza mwamva nkhawa yathu, tiuzeni pame-
ne mwaima.
Tiyi wopanda zida: Tiyi wopanda chomwera.
Chitsanzo: Akungomwa tiyi wopanda zida.
Tola m’kamwa: Kufufuza zolakwa m’zokamba za anthu.
Chitsanzo: Amabwera kuno kuti adzangonditola m’kam-
wa.
Tola nkhwangwa ndi mpini womwe: Chita mwayi
waukulu kwambiri.
Chitsanzo: Anzathu mwatola nkhwangwa ndi mpini wom-
we, kodi munasamba pati?
355