Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 355

Paphata pa Chichewa Thupi lozuka: Thupi lofutukuka, munthu wathupi lalikulu. Chitsanzo: Mayi awo ali ndi thupi lozuka. Thushula: Menya kwambiri, panda. Chitsanzo: Anzake amuthushula. Thyola bano: Kutha msinkhu, kuyamba kusamba kapena kutulutsa umuna. Chitsanzo: (1) Mwana ujatu wathyola bano chaka chathachi. (2) Wayamba kuchita manyazi kwambiri, ndikukhulupirira kuti wathyola bano. Thyola khola: Kusiya mkazi wako n’kumakagona kapena kukakwatira wina. Chitsanzo: Bambo aja anathyola khola n’kupita m’mudzi wapamtundapo. Thyola m’nkhongono: Kutha mphamvu Chitsanzo: Sindinayembekezere kumva zimenezi moti mwandithyola m’nkhongono. Thyola mtima: Kukhumudwa. Chitsanzo: Zimene achitazi zandithyola mtima. Thyolera m’kamwa: Kudya. Chitsanzo: Ndipatse bakhayu ndikathyolere m’kamwa. Thyolera m’thumba: Ika ndalama m’thumba. Chitsanzo: Atangolandira zake anazithyolera m’nthumba. Thyolera: (a) Kukhala wopirira. Chitsanzo: Ngati ukufuna ukakhala bwino pamudzi pamene paja, uzikangothyolera ngakhale akunyoze. (b) Kugona. Chitsanzo: Mlondayo anamupeza akuthyolera. Thyoletsa bande: Thamangitsa. Chitsanzo: Ukapitiriza kushashalika adzakuthyoletsa bande. 354