Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 354

Paphata pa Chichewa Thudzula gule: Kumenya munthu kapena kuchita ndewu. Chitsanzo: Akachita masewera tithudzula gule. Thudzula: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Akapitiriza kundiputa ndimuthudzula. Thukuta liri kamukamu: Ali thukuta lokhalokha. Chitsanzo: Ndinakumana nawo ali thukuta kamukamu. Thula: Khala chete. Chitsanzo: Thula! Wati amanena chiyani? Thumba lobooka: Mawuwa amanenedwa pofotokoza munthu amene sasunga ndalama. Chitsanzo: Mavuto andichulukira moti ndikugwira ntchito molimbikira koma ndikungokhala ngati ndikulandirira ndalama m’thumba lobooka. Thumuka: Kuduka kwa ulusi kapena chingwe. Chitsanzo: (1) Ulusiwu suchedwa kuthumuka. (2) Tathumulani ulusi wangoti yaviyaviwo. Thunga: (1) Kalichero kakang’ono. Chitsanzo: Apakulira nsima m’kathunga. (2) Dzina la njoka. Chitsanzo: Panadutsa thunga apa. (c) Munthu wokonda kukhala m’nyumba. Thunga ndi njoka imene imakonda kukhala kuuna wake osatuluka kunja. Chitsanzo: Nankhoma ndi thunga, amachita manyazi kukhala pagulu la anthu. Thunza mtima: Dekha. Chitsanzo: Thunzani mtima achimwene, musapupulume. Thupi (chithupi): Kunenepa. Chitsanzo: Mayi awo ndi a thupi. Thupi lolagala: Thupi lokhwima. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi thupi lolagala. 353