Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 352
Paphata pa Chichewa
Thawa mfuwu wake womwe: Kudabwa zimene wanena
wekha.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani amathawa mfuwu wake
womwe?
Thawitsana: Kutengana kwa mwamuna ndi mkazi
n’kupita kutali n’kumakakhala limodzi monga banja.
Chitsanzo: Anathawitsana ndi mwamuna wa eni.
Theka:
(a) Kugwidwa.
Chitsanzo: Mbava imatibera ija yatheka lero.
(b) Kutoperatu.
Chitsanzo: Anawa atheka, pitani mukawagoneke.
Thendo:
(a) Mtedza kapena zinthu zokometsera ndiwo kapena
chakudya china.
Chitsanzo: Mundiwozi atsiramo thendo.
(b) Mawu kapena nkhani yongowonjezera.
Chitsanzo: Munkhaniyi awonjezeramo thendo.
Thephethephe: Chamadzimadzi.
Chitsanzo: Waphika nsima yathephethephe.
Thima:
(a) Kumwalira.
Chitsanzo: (1) Chigawenga chija chathima. (2) Limbikira
kugwira ntchito kuti ukadzathima, tidzagawane chuma
chakochi.
(b) Kuledzera kwambiri.
Chitsanzo: Amangodzikodzera akathima.
(c) Kusiya kuganiza, amakhala ngati sakudziwa chimene
chikuchitika, amasokonezeka.
Chitsanzo: Bambowa nthawi zina amathima.
Thimbwidzika: Kuyenda monyada, kuvina kwambiri.
Chitsanzo: (1) Ndinakumana nawo akuyenda moth-
imbwidzika. (2) Ndinawapeza akuthimbwidzika.
351