Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 351

Paphata pa Chichewa Tenthatizime: Munthu woyambanitsa anthu. Chitsanzo: Pamudzi pano pali tenthatizime. Tepatepa: Kupanda mphamvu, kutalika kwambiri. Chitsanzo: Akamayenda amangoti tepatepa. Thabza mitambo: Kungochita zinazake pofuna kupusitsa anthu kuti achoke, inuyo mukumanenso. Chitsanzo: Titaona kuti pachuluka anthu, tinabalalika mothabza mitambo. Timafuna enawo achoke kuti tikumane tokhatokha. Thamanga: Kugona ndi amuna kapena akazi ambiri. Chitsanzo: (1) Mkazi amene uja ndi wothamanga. (2) Wafatsa panopa, pakatipa anathamanga zedi mtsikana ameneyu. Thamangira kumatenda: Yendera odwala. Chitsanzo: Ndikuthamangira kumatenda, amalume ad- wala. Thambitsa (thamba): Langidwa, theka. Chitsanzo: Mpofunika kumuthambitsa mwana ameneyu. Thambo: Dothi lakumanda. Chitsanzo: Pofuna kukhaulitsa anamfedwa, adzukuluwo anatenga thambo n’kukaliika kunsewu. Thandala: Malo oyanikapo mbale. Nthawi zambiri amamangidwa ndi mitengo. Chitsanzo: (1) Ayanika mbale pathandala. (2) Tipange thandala loyanikapo nsomba. Thaphya: Kugona kapena kukhala pansi moti sungadzu- kenso wekha. Chitsanzo: Anamupeza ali thaphya, mowa uli m’mutu. Thasathasa: Chophwamphwanthika, chafulati. Chitsanzo: Chitumbuwa chimafunika kukhala chathasathasa. 350