Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 350

Paphata pa Chichewa wanuyu ndi wotengeka ndi zinthu. Tengera kuchala: Nyoza. Chitsanzo: Osamalola kuti anthu azikutengerani kuchala. Tengera kumtoso: Kunyoza, kululuza, kuchepetsa. Chitsanzo: Sindifuna zonditengera kumtoso! Tengera kunyanga: Bwera naye pamodzi. Chitsanzo: Ndinaganiza zongowatengera kunyanga. Tengera nkhali: Kulandidwa mkazi. Chitsanzo: Iwo ankangoyendayenda moti mnzawo anawatengera nkhali yawo. Tengera pamgong’o: Kunena za munthu wina zomwe sukuzidziwa bwinobwino. Chitsanzo: Ndimadana ndi anthu oti azinditengera pamgong’o. Tengera pamwamba: Fotokoza zimene sunazimve bwino. Chitsanzo: Ungachite bwino kumvetsera zimene akunenazi kuti usazitengere pamwamba. Tengera phuma: Kuchita zinthu mofulumira kwambiri. Chitsanzo: Amene uja si wofunika kumutengera phuma, akupwetekani! Tengetsa: Kupanikiza chinthu kapena munthu pomufunsa mafunso kapena kumuthamangitsa. Chitsanzo: Anzake anamutengetsa. Tengulira: (a) Kudulira. Chitsanzo: Ndipita kukatengulira maluwa. (b) Kusamalira chinthu. Chitsanzo: Mpofunika ndikatengulire ntchito yanga. Tenthana moto m’nyumba: Akulongolozana. Chitsanzo: Pakangotha chaka, anthu okwatirana ama- yamba kutenthana moto m’nyumba. 349