Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 35

Paphata pa Chichewa Chiledzerere: Munthu amene nthawi zonse amangokhala woledzera. Chitsanzo: Kodi chiledzerere chija chili kuti? Chilengwalengwa: (a) Chinthu chomwe si chenicheni. Chitsanzo: Chimene mwaonacho ndi chilengwalengwa. (b) Munthu wopanda pokomera, wopanda ntchito. Chitsanzo: Chilengwalengwa chija chinabweranso kudzapempha lero. Chiletso: Wovuta kwambiri, wotopetsa. Chitsanzo: Mwana uyu ndi chiletso. Chilombo: (a) Gule. Chitsanzo: Chilombocho atachiitanira kanyenya, chinatenga kuti chikadyere nsima kunyumba. (b) Munthu wamphamvu yemwe mwina amakonda kumenya anzake. Chitsanzo: Palime amene sadziwa kuti munthu amene uja ndi chilombo. (c) Munthu woipa mtima yemwe samva chisoni anzake akamazunzika. Chitsanzo: Amene aja ndi chilombo ndithu, zoona kumangoonerera mwana wawo akufa ndi njala? (d) Munthu waluso kwambiri Chitsanzo: Amene uja ndi chilombo cha masamu. (e) Munthu wankhanza. Chitsanzo: Ndani angakonde kukwatiwa ndi chilombo ngati chimene chija. Chimanjamanja: Kuyenda osatenga kanthu. 34