Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 349
Paphata pa Chichewa
(b) Kuoneka wotsika kapena wotsalira.
Chitsanzo: Akuona kuti atchipa akapita wapansi.
Tchitchi: Fungo la zinthu zomwe zapserera pansi pampo-
to.
Chitsanzo: Pepanitu, ndiwo zakezi zikununkha tchitchi.
Telala: Munthu wokonda akazi.
Chitsanzo: Bambo awa ndi telala.
Tema: Kupha anthu.
Chitsanzo: Matenda a malungo akutema anthu ochuluka.
Tembenu, nkhongo gwa, ulendo: Kuchoka motsimikiza,
mosayang’ana m’mbuyo.
Chitsanzo: Atamaliza kulalata, anangoti tembenu, nkhongo
gwa, ulendo!
Tembenuka: Lapa, siya kuchita zoipa.
Chitsanzo: Amene akufuna kudzapulumuka ayenera
kutembenuka.
Tenderera nkhani: Kuwonjezera zina ndi zina munkhani.
Chitsanzo: Anthu amakonda kutenderera nkhani?
Tenga mtima (koka mtima): Kukusangalatsa n’kufika
potengeka nayo.
Chitsanzo: Nyimboyi yanditenga mtima.
Tengana chulu chathyula: Kutsata munthu
m’modzimozi.
Chitsanzo: Adatengana chulu chathyula.
Tengana:
(a) Kukwatirana
Chitsanzo: (1) Mnyamata ndi mtsikana uja atengana. (2)
Angoganiza zongotengana popanda kuchita ukwati.
(b) Yendera limodzi.
Chitsanzo: Atengana, alowera uku.
Tengeka: Kusachedwa kukopeka ndi chinthu.
Chitsanzo: (1) Anthu ena ndi otengeka zedi. (2) Mwana
348