Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 347
Paphata pa Chichewa
Tambala: Mwamuna.
Chitsanzo: Atambala awiri a pamudzipo amasosolana
chifukwa cholimbirana mkazi.
Tambalala: Kukhazikika. Mawuwa amatanthauzanso ku-
khala moongola miyendo.
Chitsanzo: (1) Sikuti mubwere pakhomo pano kudzatam-
balala. (2) Kodi mwachita kutambalala? Pajatu amati mu-
sachedwe!
Tamula:
(a) Kutchula dzina la munthu kapena chinthu
chinachake.
Chitsanzo: Onse afika, kupatulapo amene mwatamulawo!
(b) Kukoka chnthu kuti chitalike kapena kufutukuka.
Chitsanzo: Tatamulani lambayu.
Tapa m’kamwa: Kufunafuna zolakwa pa zomwe wina
akunena.
Chitsanzo: Sikutu akundifunsa kuti adziwe, akungofuna
kunditapa m’kamwa.
Tapatapa:
(a) Atagoneratu.
Chitsanzo: Ndinamupeza ali tapatapa.
(b) Mvekero wofotokoza zinthu zofewa.
Chitsanzo: Mapeyala onse ali tapatapa.
Tatede: Ndalama. Angagwiritsidwenso ntchito ponena zin-
thu zina zimene simukufuna kuti anthu azidziwe.
Chitsanzo: Tatede wako ndamuika pansi pa mtsamiro.
Tatimasuleni: Tatiuzeni bwinobwino.
Chitsanzo: Tatimasuleni, mukutanthauza chiyani?
Taya bomwetamweta: Taya mwayi.
Chitsanzo: Akupusitsani kwambiri. Akutaitsanitu bomwe-
tamweta!
346