Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 346
Paphata pa Chichewa
Takasa: Kusokoneza zinthu.
Chitsanzo: Bwana woyamba anangotakasa zinthu n’ku-
chokapo.
Takata:
(a) Gulitsa kwambiri.
Chitsanzo: Koma ndiye mwatakatatu lero!
(b) Kukhala ndi khalidwe lachimasomaso.
Chitsanzo: Watakata amuna ambiri mkazi ameneyu.
Takataka: Gwira ntchito, phika chakudya.
Chitsanzo: (1) Mkazi amafunika azitakataka. (2)
Musachoke, mayi akutakataka kuseriku.
Takuonanitakuonani! Mawu aulemu omwe anthu
amanena akamadutsa munthu. Mawuwa ayamba kulowa
m’malo mwa “wawa.”
Chitsanzo: Takuonanitakuonani! Kaya muli bwanji?
Talikira:
(a) Suntha pano.
Chitsanzo: Talikira, ndingakukankhe.
(b) Kuchokapo kupita kwina.
Chitsanzo: Amenewo simunawapeze, atalikira!
Tama ine: Yamika ine.
Chitsanzo: Uzitama ine, zikanakuvuta ndikanapanda
kukhalapo.
Tama mano: Tama nzeru, chuma, mphamvu ndi zina
osati za wina.
Chitsanzo: Ukamafuna kuchita chinachake, umatama
mano.
Tamba: Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito aka-
manena zokhudza zikhulupiriro za ku Africa kuno zo-
khudza ufiti.
Chitsanzo: (1) Mfiti zojaira zimatamba masanasana. (2)
Akungokhala ngati awagwira akutamba.
345