Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 344
Paphata pa Chichewa
Sumbudzula: Kumenya, kukhaulitsa.
Chitsanzo: Ukabweranso usiku ndikusumbudzula.
Sunga khosi: Pirira zokoma zikubwera.
Chitsanzo: Ngati ukufuna udzakhale ndi tsogolo labwino,
sunga khosi. Nanga ungadzavale mkanda woyera khosi
ulibe?
Sunga mwana: Sunga zinthu zofunika kwambiri, thawitsa
zako. Mawuwa amanenedwa choopsa chikamabwera.
Chitsanzo: Zikakuvuta ukhoza kugulitsa zonse, koma
osaiwala kusunga mwana.
Sungakhumbire: Sungasirire, sungazifune.
Chitsanzo: Sungamukhumbire utaona zimene amachita.
Sungulumwa: Kusowa wocheza naye.
Chitsanzo: Mukachokapo ndimasungulumwa.
Sunsunuka: Kukula.
Chitsanzo: Tsopano mwasunsunuka, mukufuna
mutisowetse mtendere.
Sunyenyeka: Suvutika kapena kumva kupweteka.
Chitsanzo: Ngakhale chibwenzi chitatha, sind-
inganyenyekeyi.
Sunzumira anthu: Kukaona anthu kwa nthawi yochepa.
Chitsanzo: Ndakhalitsa m’tauni muno, mpofunika ndipi-
teko kumudzi ndikawasunzumire anthu.
Supula: Kuputa mkwiyo kwambiri.
Chitsanzo: Andisupula, adziwanso kuti ndine Nasimango.
Suwa: Kuchoka kapena kuperepeseka kwa khungu.
Chitsanzo: Khungu lawo likusuwa.
Swera mphanje: Kuwonjezera mabodza.
Chitsanzo: Usamachite kufotokoza moswera mphanje.
Swetsa mutu (iswa mutu): Chopatsa maganizo kwambiri,
kuganiza mozama.
Chitsanzo: Nkhani imeneyi ikundiswetsa mutu.
343