Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 343
Paphata pa Chichewa
Sowa yamchere (yasopo): Kusowa ndalama, kuvutika.
Chitsanzo: Azibusa ambiri akudya bwino, koma nkhosa
zawo zikusowa ndi yamchere yomwe.
Sowa zochita:
(a) Kumangoyendayenda, kumangochita zinthu
zosafunika kwenikweni.
Chitsanzo: Chifukwa cha kusowa zochita anthu ambiri
amavala gule.
(b) Kukhala popanda ntchito yoti ugwire.
Chitsanzo: Dzulo ndimasowa chochita.
Sudziwa mtima wamoto: Sudziwa zomwe zitachitike,
mwina chipserera.
Chitsanzo: Papsa tonola sudziwa mtima wamoto.
Sudzula: Kuuzidwa kuti udzipita kwanu banja litatha.
Chitsanzo: Powasudzula anawapatsa 3 kwacha n’kuwau-
za kuti adzipita kwawo.
Sukulu yamkaka: Sukulu ya ana aang’ono kwambiri.
Anazipatsa dzinali chifukwa anawo amamwa mkaka.
Chitsanzo: Boma latsegula sukulu zamkaka.
Sukulu yankombaphala: Sukulu ya ana aang’ono.
Chitsanzo: Chaka chamawa akayamba sukulu
yankombaphala.
Sula mwana: Kuphunzitsa mwana makhalidwe abwino.
Chitsanzo: Ana anuwa munawasula bwino.
Suluka:
(a) Kuchoka mtundu.
Chitsanzo: Nsaluyi ndi yosuluka.
(b) Kutha mphamvu.
Chitsanzo: Mankhwalawa anasuluka.
Sumbudzuka: Ng’ambika, sosoka, fwifwa. Angatan-
thauzenso kubwera usakuoneka bwino.
Chitsanzo: (1) Andipatsa malaya osumbudzuka. (2)
Abwera atasumbudzuka.
342