Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 342

Paphata pa Chichewa Solola ndalama: Kuba ndalama zochepa. Chitsanzo: Ena akamapakula ndalama, ena amangosolola pang’ono. Sololoka mlomo: Munthu wa mlomo waukulu. Chitsanzo: Amakonda kutsonya, n’chifukwa chake ali wosololoka mlomo. Songo: Munthu wabwino pamaso, koma kuseri amakukonzera chiwembu kuti akuphe kapena kukunenera mabodza. Chitsanzo: Chenjerani, munthu ameneyu ndi songo. Sosolera pamsampha: Chenjeretsa. Chitsanzo: (1) Sindifuna kuchita zinthu ndi ameneyu, amakonda kusosorera pamsampha. (2) Mnyamata ameneyu amakonda kusosolera pamsampha. Sosora nthenga: Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene anali ndi udindo kapena mphamvu zinazake ndiye mphamvuzo zinatha kapena ena anamuchotsera mphamvuzo. Chitsanzo: Ife anatisosora nthenga, sitilinso ndi mphamvu ngati kale. Sowa chochita: Sowa chonena, kungokhala osachita kanthu. Chitsanzo: Atamupanikiza ndi mafunso, anangoti nyotcholo, kusowa chochita. Sowa cholaza: Kutsatira khalidwe lolakwa la kumaloko. Chitsanzo: Ukapita pa mudzi wa zidakwa, umasowa chola- za. Sowa pogwira: Kusowa chochita pamavuto. Chitsanzo: Matenda akalowa pakhomo umasowa pogwira. Sowa tulo: Kukuvutika maganizo koopsa, kuchititsa kuti usagone. Chitsanzo: Nkhaniyi imamusowetsa tulo. 341