Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 341

Paphata pa Chichewa Sisitira bondo: Zengereza. Chitsanzo: Ukasisitira bondo anzako atenga. Siwa: Nyumba yamasiye. Chitsanzo: Titapita kumaliroko, tinauzidwa kuti tikagone ku siwa. Koma si nsikidzi tinazipeza kumenekozo! Siya fumbi lili kobo: Thawa, yendetsa galimoto mofu- lumira kwambiri. Chitsanzo: Amayendetsa ngati waledzera, moti anangosiya fumbi lili kobo! Siya kafumbu: Mwalira. Chitsanzo: Amalume awo asiya kafumbu. Siya phazi: Usamakonde kuyankhulayankhula. Chitsanzo: Nditayamba kubwebwetuka, anangondichenje- za kuti: “Siya phazi, ukasiya pakamwa padzakutsata!” Sizinthu (sikanthu): Chopanda ntchito, munthu wachachabechabe. Chitsanzo: Mayi amene aja sizinthu! Soka mphasa: Kugona chifukwa cha matenda. Chitsanzo: (1) Masiku ano sakupeza bwino, akumangosoka mphasa. (2) Sabata imeneyi ndimasoka mphasa. Sokolotsa: (a) Vumbulutsa, thamangitsa. Chitsanzo: Onse amene anabisala awasokolotsapo. (b) Angatanthauzenso chimene chachititsa munthu kuchoka kwinakwake. Chitsanzo: Chakusokolotsani m’taunimo n’chiyani? Sokoneza mutu: Kubalalitsa, kukupangitsa kuti usowe chochita. Chitsanzo: Nkhaniyi yandisokoneza mutu. Solola mulomo: Kutsonya. Chitsanzo: Ndinadziwa kuti akazi awo akwiya koopsa chifukwa pamene amachoka anangosolola mulomo. 340